Jubilee Year of Mercy Indulgences

Chaka Choyera cha Jubilee chilli ndi maziko ake. Powerenga Baibulo timamva kuti mawu oti Jubilee amachokera ku mawu oti Yobel.  (Levitiko 25:10-14) Yobel inali nyanga ya mbuzi imene amailiza ngati lipenga lolengeza kubwera kwa chaka cha padera cha Ayuda. Patapita nthawi, chaka cha paderacho adachitcha Jubilee.

Amachita zotani pa Chaka cha Jubilee?

1.      Ngati adatenga malo ngati chigwiriro adayenera kubweza kwa mwini wake m’chaka cha Jubilee.

2.      Ngati adali ndi ngongole ndi ena adayenera kuikhululukira ngongoleyo.

3.      Adayenera kukhuluka ndi kumasula am’ndende

4.      Adayenera kusalima chaka chimenecho kuti nthaka ipume.

 

Chaka cha Jubilee chidafika pachimake pake ndi Ambuye Yesu pamene adalengeza kuti: Mzimu wa Chauta wadzaza mwa Ine.

Wandidzoza kuti ndikalalikire amphawi Uthenga Wabwino.

Wandituma kuti ndikalengeze kwa am'ndende kuti adzamasulidwa,

ndi kwa akhungu kuti adzapenyanso. Wandituma kuti ndikawapatse ufulu anthu osautsidwa, ndi kukalalika za nthawi imene Ambuye adzapulumutsa anthu ao." (Luka 4:18-19)  Nthawi yopulumutsa anthu awo ndi imene tikuitcha tsopano Jubilee ya Ambuye Yesu.

 

Mpingo wathu pophunzitsa za Jubilee ukutiuza kuti Chaka Choyera cha Jubilee ya Chifundo chikutipatsa mwawi:

Wa chikhululukiro cha chilango chobwera chifukwa cha machimo athu ngakhale tawalapa kale ngati moyo wathu ukukhalabe mu chaulere choyeretsa, chimene mpingo umapereka kwa akhristu amene agwira ntchito zoyeretsazi ndi chithandizo cha Ambuye Yesu ndi Oyera awo. CIC 992, CCC1471 (Indulgences)

 

Mbiri ya  Chaka Choyera cha Jubilee

 

Ma Jubilee a mtundu woterewu adayamba m’chaka cha 1300 ndi Papa Boniface VIII. Kuyambira nthawi imeneyi mpingo wakondwelera ma Jubilee okwana 26 ndipo Zaka zina Zoyera zapaderadera (extraordinary jubilee) zakwana zitatu. Chaka ichi cha Jubilee ya Chifundo ndi chachinayi.

 

Chaka Choyera chimatipatsanso mwawi:

1.      Woyanjana ndi amene tidasiyana nawo maganizo

2.      Wotembenuka mtima kwathunthu

3.      Wolandira Sakramenti la kulapa moonadi ndipo pafupipafupi

4.      Wokulitsa umodzi, chiyembekezo, chilungamo ndikudzipereka ku utumiki wathu mwachimwemwe poyesetsa kukhala mwa bata ndi mtendere ndi abale ndi alongo athu.

 

Chaka choyera cha Jubilee ya Chifundo koposaposa ndi chaka choyenda ndi Ambuye Yesu amene akutipatsa moyo ndi zaulere zofunikira pa umunthu wathu.

 

Zokhululukira za padera za Eklezia  (Indulgences)

 

Uku ndi kukhululukira kwa chilango chobwera chifukwa cha machimo athu ngakhale tawalapa kale ngati moyo wathu ukukhalabe mu chaulere choyeretsa, chimene mpingo umapereka kwa akhristu amene agwira ntchito zoyeretsazi ndi chithandizo cha Ambuye Yesu ndi Oyera awo. CIC 992, CCC1471

 

Kudzera mu dongosololi tonse timakumana ndi chifundo cha Mulungu amene amatilandira, amatikhululukira ndipo amaiwala kwathunthu machimo omwe tidawachita.

 

Zoyenera kuchita M’chaka Choyera cha Jubilee ya Chifundo.

 

1.      Kudutsa pakhomo la Chifundo ku matchalitchi ndi malo onse amene atchulidwa kuti ndi Oyera.

2.      Kuyenda Maulendo Oyera. (Pilgrimages)

3.      Kuchita imodzi mwa ntchito yachifundo yathupi kapena ya uzimu kamodzi patsiku.

4.      Kuwerenga ndi kusinkhasinkha Malembo Oyera makamaka Mthenga Wabwino wa Luka Woyera.

5.      Kuchita chidwi ndi kudziwa moyo wa anthu Oyera

6.      Kulekana ndi machimo athu aakuluakulu ndi aang’ono omwe

7.      Kulapa ndi kuulula machimo athu kwa Wansembe kawirikawiri

8.      Kulandira Ukalistia

9.      Kukhazikika mu chaulere cha Mulungu

10. Kupempherera Pemphero la Kumvera kwa Apostoli

11. Kupempherera zolinga za Apapa. Atate athu, Tikuoneni Maria ndi Ulemu

 

Tichite zotani tikafika ku Malo amene akhazikitsidwa kuti ndi Oyera?

 

1.      Ngati nkotheka tichite mdipiti wolowera pakhomo la Jubilee ya Chifundo. Titha kumaimba nyimbo za chifundo kapena kupemphera Litania la Oyera Onse.

 

2.      Tipemphe kulandira Sakramenti la Kulapa.

 

3.      Titha kuchita mapemphero awa:

a.      Njira ya Mtanda

b.      Kolona ya Chifundo

c.      Kupembedza Ukalistia(mkati mwake tiwerenge Malembo Oyera kapena tichite Kolona ya Amai Maria komanso tipereke nthawi yokhala chete pa maso pa Ambuye Yesu Wokhala mu Ukalistia (mphindi 15)

 

4.      Tichite nawo nsembe ya Ukalistia. Ngati ndi nthawi ya Ulendo Woyera ansembe athandize kuti akhristu alandire Ukalistia umene wasandulitsidwa pa Nsembe ya Ukalistia imeneyo. Tithanso kuchita nawo Nsembe za Ukalistia zina ngati nthawi imene tinayenda ulendo woyera kunalibe Nsembe ya Ukalistia koma ndi cholinga chofuna kukwaniritsa dongosolo la Chaka Choyera cha Jubilee ya Chifundo.

 

5.      Tipereke za chifundo ngati gulu kwa amene tasankha kapena kupatsira ena amene tikudziwa kuti atha kupereka zachifundozo monga takonzera monga kwa ansembe kapena asisiteri ndi ena.

 

Kodi ntchito zachifundo tikunenazi ndizo ziti?

 

Ntchito za Chifundo za Uzimu

1.      Kuphunzitsa amene ali osadziwa

2.      Kulangiza ndi kuunikira amene akukaikakaika

3.      Kuwadzudzula ochimwa

4.      Kupilira zolakwa modekha

5.      Kukhululukira ena ndi mtima wonse

6.      Kuthunzitsa mtima amene ali osweka mtima ndi amene akulira

7.      Kupempherera amoyo ndi akufa.

 

Ntchito zachifundo zathupi (zooneka ndi maso) Mateo25:31-46

1.      Kudyetsa anthu anjala

2.      Kupatsa madzi amene ali aludzu

3.      Kuveka amene ali amaliseche

4.      Kupezetsa malo amene alibe pokhala

5.      Kuyendera anthu a kundende

6.      Kuchezera odwala

7.      Kuika nawo Maliro

 

 

Presentation by Fr. E. Kanjira